Chichewa Christian Hymns
Hymn 96 MTIMA wanga uyamiketu,
MTIMA wanga uyamiketu,
Mfumu yangayo ya Kumwambako;
Mtima wanga uyamiketu,
Zokoma zake za Yesu.
Yesu, Yesu, Yesu,
Inu nokhadi;
Ndikuyamikani,
Ambuye wa moyotu.
Ndiyamike Yesu wangayo,
Anandifera anawukanso;
Andipempherera M’mwambamo,
Abweranso kutenga ‘ne.