Chichewa Christian Hymns
Hymn 49 ONA Mwanawankhosayo
ONA Mwanawankhosayo
Wakuseza zakuipa zathu zonse.
Mwana wankhosa
Watisenzera
Zakuipa zathu zonse.
Anazenza m’thupi mwake;
Pakukhomedwa pa mtanda anali duu.
Ona pamtanda Yesuyo
Anabvutika chifukwa cha anthu’fe.
Imva kulira kwa Yesu
Pamene anasiyidwa muimfayo.
M’mwazi wake tisambamo;
Zichotsedwa zakuipa zathu zonse.
(Ona Mwana wa nkhosayo
Wakusenza zakuipa, zathu zonse.)