Chichewa Christian Hymns
Hymn 257 NJIRA yanga sindiziŵa,
NJIRA yanga sindiziŵa,
’Tate muikonza;
Komatu muzindikira
Kuti mundikonda.
M’mene mantha andigwira,
Andidetsa m’mtima,
Mbuye, ndithaŵire kwanu
Poti mundikonda.
Sindidziŵatu zamaŵa,
Koma sindiopa;
Ndidzakhulupira Inu
Kuti mundikonda.
Inde wakukonda ndinu;
Mawuwo oona
Andidzaza ndi chimwemwe:
Mlungu andikonda.