Chichewa Christian Hymns
Hymn 78 ALINKUDZA wansoni Munthu,
ALINKUDZA wansoni Munthu,
Wakukhala Kumwamba;
Alinkudza m’ulemerero,
Ndi Mwamuna wa mtanda.
Aleluya, Aleluya,
Alinkudza kwa ife;
Ndi chimwemwe
Tidzamkomana,
Pakufika Ambuye.
Alinkudza Ambuye Yesu,
Wakuphedwa pa dziko;
Alinkudza kukhala Mfumu,
Yoweruza mayiko.
Pakufika asonkhanitsa,
Anthu ake oyera;
Adzafuna mitundu yonse,
Omwe Iye ‘nafera.