Chichewa Christian Hymns
Hymn 483 NTHAŴI yaubwana yatha,
NTHAŴI yaubwana yatha,
Sukulu yathu yathanso;
Nkhaŵa ndizoŵaŵa zomwe
Zitibisaliranso.
Yesu wakufatsa mtima
Mlendo pansi pano ’Ye,
’Natifera, natisunga,
Atitsogolere ’fe.
Tamverani, aitana;
“Ana, munditsatetu,”
Yesu, tisapite kwina,
Tizikutsatani ’Nu.
Posachedwa tilekana
Osalankhulananso,
Koma tidzaona tonse
Wina mnzake m’Mwambamo.