Chichewa Christian Hymns
Hymn 471 YESU Mbuye ’Nu wofatsa
YESU Mbuye ’Nu wofatsa
Muyang’anedi kamwana,
Mndichitire chifundo;
Mundilole kwanutu.
Ndimalira kwa Inutu,
Mpatse mtimawo wabwino;
M’Dziko lanu loŵalalo
Mulandire mwana wanu.
Yesu, E, ndikufunani,
Ndinu chuma change chonse;
Mtima wanu ngwofatsadi;
Kale munali kamwana.
Wonga Inu ndikhaledi,
Mtima wanu mundipatse;
Yesu ndinu wokomatu,
Mndiphunzitse kukonda ’Nu.
Yesu Mbuye ’Nu wabwino,
M’manja mwanu ndikhalemo;
Mzimu wanu mundipatse,
M’khaletu mtima mwangamu .