Chichewa Christian Hymns
Hymn 414 INU bambo, inu mayi,
INU bambo, inu mayi,
M’tsateni Mbuye m’tsateni;
Adziwa zinsinsi zanu,
M’tsateni Mbuye m’tsateni.
Anapeza mavutowo,
Napereka moyo wake,
Namwa ndulu m’malo mwathu;
M’tsateni Mbuye m’tsateni.
Anyamata, atsikana,
M’tsateni Mbuye m’tsateni;
Adziwa zinsinsi zanu,
M’tsateni Mbuye m’tsateni.
Anthu onse a padziko,
M’tsateni Mbuye m’tsateni;
Adziwa zinsinsi zanu,
M’tsateni Mbuye m’tsateni.