Chichewa Christian Hymns
Hymn 363 ATATE ndiyamika,
ATATE ndiyamika,
Mwandisamalira leroli;
Mulungu wandikonda,
Mndisungenso m’mdima muno bii.
Mundikumbutse, ndikapanda tulo,
Za Kumwambako;
Zoganizira, zoipitsa,
M’mtima muchotseremo.
Zochimwa za usana uno
Mndikhululukire ’ne;
Mtendere wanu muloŵetse;
M’mtima ndikagone phee!
Mundilimbitse ndikayese,
Manda ngati mphasayi,
Nditagonamo ndikadzuke,
Tsiku lomalizalo.
Tiyamike Mlungu wotipatsa,
Zachifundozi;
Amyamikire onse,
A Kumwamba ndi apansipa.