Chichewa Believers Christian Hymns
Hymn 1791 Tiimbe nyimbo zotamanda
Tiimbe nyimbo zotamanda
Mulungu wathu wabwino,
Pakuti akondana nawo
Anthu okhala padziko;
Tero natuma Mwana wake,
Wakukondedwa kalelo,
Kutiphunzitsa ife tonse
Za chikondano chakecho.