Chichewa Christian Hymns
Hymn 9 TAMANI Ambuye,
TAMANI Ambuye,
Wamphamvu ndi Iye;
Akhala m’ulemu,
Kumwamba komweko.
Chikopa cholimba,
Ndi kothaŵiranso;
Kwa anthu akewo,
Kotero ndi Mlungu.
Uzani zamphamvu,
Imbani chisomo;
Za Mwini ulemu,
Ambuye wathuyo.
Poomba chimphepo
Mvulanso ndi bingu;
Padziko, pathambo,
Akhala ponsepo.
Zozizwa zam’dziko,
Za M’mwamba zonsezi;
Mulungu wamphamvu,
Munalenga zonse;
Muyendetsa mwezi,
Nyenyezi ndi dzuŵa;
Zolengedwa zonse,
Zimvera Ambuye.
Sitiha ifedi,
Kukamba zokoma;
Za Inu Mulungu,
Wolera anthuwa.
Zifika ndi mphepo,
Ndi mvula ndi dzuŵa;
Zigwera ponsepo,
Pa anthu onsewa.
Wamphamvu yosatha,
Chikondichangwiro;
Angelo akonda,
Kutama Mulungu.
Ndiponso ifetu,
Ana ‘nu tonse ‘fe;
Tiimba nyimboyi,
Yotama Ambuye.