Chichewa Christian Hymns
Hymn 420 FESANI mbewuzo,
FESANI mbewuzo,
Mbewu zabwinozo;
Fesani mbewuzo,
M’dziko lapansi.
Fesani mbewuzo, mbewu zabwinozo;
Fesani patali, ndi dzanja lokoma.
Ndi kunyema mkate
Ndi kulalika Mawu,
Fesani mbewuzo, m’dziko lapansi.
Fesani mbewuzo,
Nthawi yam’mamawa;
Fesani mbewuzo,
M’dziko lapansi.
Fesani mbewuzo,
Nthawi yamadzulo;
Fesani mbewuzo,
M’dziko lapansi.
Fesani Uthenga,
Uthenga wabwino;
Fesani Mawuwo,
M’dziko lapansi.
Fesani Mawuwo, mawu a Yesuyo,
Fesani patali, ndi dzanja lokoma;
Ndi kulalikira mawu a
Mulungu wathu,
Fesani Mawuwo m’dziko lapansi.