Chichewa Christian Hymns
Hymn 34 AMITHENGA a Mulungu,
AMITHENGA a Mulungu,
Anaimba nyimbo yomwe,
Posonkhana m’mlengalenga,
Natitu usiku womwe;
“Onse azilemekeza
Mlungu Wakumwambamwamba;
Akhalebe ndi mtendere
Anthu ali ponseponse.”
Amithenga anaimba
Ndi usiku m’mlengalenga.
Anamva abusa omwe
Anaŵeta nkhosa zawo.
Mthenga nati:
“Musaope;
Mumve ndikufotokoza:
Wabadwa usiku uno Yesu Kristu Ambuyathu
Ndiye Mpulumutsi wathu;
Anabadwa m’Betlehemu.”
Amithenga anaimba
Ndi usiku m’mlengalenga.
Yesu ndinu Mbuye wathu,
Munasiya za Kumwamba;
Munakhala mwana kuno;
Mnatifera mwaufulu.
Inu nonse amithenga,
Inu mumtamande Iye;
Anthu onse ali pansi Adza akondane naye.
Zoonazi amithenga
Anaimba m’mlengalenga.