Chichewa Christian Hymns
Hymn 123 MULI ndi ludzu, idzani
MULI ndi ludzu, idzani
Kumadzi amoyo
Imwani monse kolere
Kuchitsime konko.
Munka kangati kulaŵa
Madzi onyengera?
Musataye mphamvu yanu,
Musataye chuma.
Imvani, Yesu akuti;
“Chuma ndili nacho,
Landirani, yemwe amva
Akhale ndi moyo.”
Funani Mlungu tsopano.
Akulindirani;
Iye ndiye wachifundo,
Akulandirani.
Ali wokhululukira;
Imvani ananu:
Mtima wake usiyana
Ndi mitima yathu.
Monga m’Mwamba mupambana
Zonse pansi pano;
Choncho maganizo ake
Apitira athu.
Anthu onse a padziko
Adzamvera Mlungu:
Adzakhala ndi chimwemwe,
Nadzamtama ndithu.