Chichewa Christian Hymns
Hymn 469 NDIKONDA mbiri yomwe
NDIKONDA mbiri yomwe
Ya amithengawo
Ya Mbuye, Mfumu yathu
Pofika pansipa;
Zochimwa zindizinga,
Koma ndidziŵatu
Anawombola ine
Pakundikondadi.
Ndikondwa kuti Yesu ’Nakhala mwanatu,
Chitsanzo atipatsa
Cha moyo wakewo;
Ndikati ndimtsatire
Zochita zakezo,
Sadzandinyoza konse
Pakundikondadi.
Pakumyamika Iye
Ndidzamwimbiratu;
Ngakhale sindimwona
Amandimveradi;
Pakuti walonjeza
Adzalandira ’ne
Ndiimbe ndi angelo,
Pakundikondadi.