Chichewa Christian Hymns
Hymn 457 KALE m’mzinda wachifumu
KALE m’mzinda wachifumu
Munalimo m’kholamo,
Momwe mkazi anaika
Mwana wake m’ndyeromo.
Ndiye mkaziyo Mariya,
Yesu Kristu Mwanayo.
Uyu ’natsikira kuno,
Mlungu Mbuye wathuyo;
Anabadwa uyu m’khola
Anagona m’ndyeromo.
Mwa osoŵa ndi oipa
Yesu anakhalamo.
Mwa ubwana wake wonse
Anakula m’mtima phee!
Anakonda, anafatsa,
Amay’ wake namvabe;
Ndipo ana nonsenu,
Mukamtsate bwinotu.
Ndipo Mwana uyu Yesu
Anakulakulabe;
Ndi wamng’ono ndi wofoka,
Anagona enawo.
Nsoni zathu anazimva
Ndi chimwemwe chathunso.
Ndi chifukwa atikonda,
Tidzampenya masowa,
Kuti Mwanayo wofatsa
Ndiye Mwini m’Mwambamo;
Atengera ana ake
Komwe adapitako.
Koma sitimpenya m’khola
Muli ng’ombe momwemo;
Ayi, tidzamwona m’Mwamba
Muli Mlungu ’Tatewo.
Ana akuyera mbuu
Adzamzunguliratu.