Chichewa Christian Hymns
Hymn 345 ATATE, ndipempha
ATATE, ndipempha
Tsopano mundimvere,
Ndipempha kuti mundithandize.
Ine ndili munthu
Wochimwa pansi pano,
Munditsuke Mbuye, ndiyeretu.
Ndalema ndathodwa
Ndi zinthu zapadziko,
Zakhalatu goli londimanga.
Yesu Mfumu Inu
Mumandiuza kuti:
“Pemphera, ndipo udzalandira.”
Ndipempha, Ambuye,
Mundidzaze n’chikondi,
Mtima wangawu ukukondeni.