Chichewa Christian Hymns
Hymn 312 NDIMAYENDA paulendo
NDIMAYENDA paulendo
Ndi yaminga njira yake;
Tsoka ndikapeza, koma
Ndinka kwa Atate;
Pena m’mtima mwanga mwada,
Pena andibvuta ‘dani,
Ndikatenga nkhaŵa, mantha,
Amadziŵako.
Ichi chindisangalatsa
M’mene nkhondo indigwira,
M’mene nsoni zazikulu
Zimanditsatira;
Mtima ukhazika m’mene
Kwathu kuja ndikumbuka
Kuti Mlungu ali ndine,
Andisungako.
Mbuye andipeza lero,
Andikonda, andisunga;
Adzapitikitsa mdani
Akamandibvuta.
E, ulendo wanga utha,
Tsono ine ndimwalira;
M’mene ndidzafika kwawo
And’landirako.
Komwe ndi chimwemwe ine
N’dzaonana ndi Atate,
N’dzagwadira ndi kumtama,
Amandikondabe.
Sakandisautsa kanthu
M’dziko lija lakukoma;
Adzandidalitsa Yesu,
Ndidzakondwako.