Chichewa Christian Hymns
Hymn 187 UFUNA kuwomboledwa kodi?
UFUNA kuwomboledwa kodi?
llipo mphamvu m’ mwazi wake;
Ufuna kugonjetsa zoipa?
Muli mphamvu m’mwazi wake.
Muli mphamvu yodabwitsatu,
M’muazi wa Yesuyo;
Muli mphamuu yodabwvitsatu,
Mmwazi wa Mwanawankhosa.
Ufuna kuleka kunyadako?
Ilipo mphamvu m’mwazi wake;
Idzatu pa mtanda nutsukidwe,
Muli mphamvu m’mwazi wake.
Ufuna kuyera kopambana?
Ilipo mphamvu m’mwazi wake;
Zoipa zonse adzayeretsa,
Muli mphamvu m’mwazi wake.
Ufuna kugwira ntchito yake?
Ilipo mphamvu m’mwazi wake:
Ufuna kumuyimbira lye,
Muli mphamvu m’mwazi wake.