Chichewa Christian Hymns
Hymn 185 NDINE Mbusayo wabwino,
NDINE Mbusayo wabwino,
Ndinafera nkhosazo;
Yotayika ndayifuna,
Mpaka ndataya moyo
Mbulu wanding’amba m’nthiti,
Wanding’ambanso m’manja,
Wanding’ambira zovala,
Ndatsala wawumphawi.
Nkhosa zanga
Zimandimva,
Ndikaziyitanazo;
Ndimazipatsa moyowo,
Atate nazisunga.
Atate wondipatsazo,
Ali nayo mphamvutu,
Kuzidyetsa, kuzisunga,
Palibe wolandazo.
Musawone zovalazo,
Mkati ali fisiyo;
Musanyengedwe anthuni,
Ine ndine Mbusayo.
Tamverani anthu inu,
Ine ndine Mbusayo,
Ndine njira, ndine khomo,
Thawani mimbuluyo.