Chichewa Christian Hymns
Hymn 179 TUMPHATUMPHA moyo wanga,
TUMPHATUMPHA moyo wanga,
Sangalala ndi Mtetezi;
Kuwombola kwa Yehova
Kwatuluka m’dziko lako.
Mulungu wakwezekatu,
Mpulumutsi m’dziko lako,
Wakwezekatu Chitetezo.
Wabvundikira iwedi
Mzimu wanga’we wafunda,
Lulutiratu moyo wanga.
Bvinabvina moyo wanga,
Lulutira mtima wanga;
Wa mawuwo a Yehova
Watuluka m’dziko lako.
Imbirira moyo wanga,
Mtendere wako wafika;
Mbendera ya Chitetezo
Waikwezetsa ndi Yesu.
Ukondwere moyo wanga,
Kuunika kuoneka,
Ndi mdimawo uthaŵatu;
Lulutira moyo wanga.
Usekere moyo wanga,
Ndi Yehova akufuna;
Wakwezatu mbenderayo
Ya Chitetezo, sekera.