Chichewa Christian Hymns
Hymn 176 AITANA, aitana dziko lonse,
AITANA, aitana dziko lonse,
Imvani mukhaliranji chete?
Aitana,
Aitana aitana dziko lonse.
Mfumu iyi, Mfumu iyi ya Kumwamba
Ndi Yesu, ndi Mpulumutsiyo wa anthu onse.
Anthu onse, anthu onse, tinke kwawo.
Aitana,aitana inu mayi,
Ndi Yesu, amene anakhetsa mwazi wake;
Mwazi wake unagwera inu mayi.
Aitana, aitana inu ’tate,
Ndi Yesu amene anakhetsa mwazi wake;
Mwazi wake unagwera inu ’tate.
Yesu ati, Yesu ati; “Muzisiye
Zoipa zimene muzichita, muzisiye,
Muzisiye, muzisiye inu nonse.”
Titi bwanji? Titi bwanji ife anthu?
Ndi Yesu anatifera ife akuchimwa;
Akuchimwa, akuchimwa tinke kwawo.