Chichewa Christian Hymns
Hymn 140 NDINAMIRA m’machimo, wosaonekanso,
NDINAMIRA m’machimo, wosaonekanso,
Ndinamira ndithudi wosatulukanso;
Koma Yesu adamva
Kulira kwangako,
Nandipulumutsa kumachimowo.
Nandikweza,
Nandikweza,
Pomira m’thopemo,
Nandikweza;
Nandikweza,
Nandikweza,
Pomira m’thopemo,
Nandikweza.
Mtima wanga ndipatsa ndidzam’kangamira,
Ndidzakhala mwa Iye ndikumuyimbira;
Mtima wanga uyimba
Za chikondi chake,
Tsono ndidzatumikira Yesuyo.
Ovutika penyani,
Yesu wolanditsa;
Adzakutulutsani
M’mafunde owopsa;
Ndiye Mwini nyanjayo, mafunde amvera;
Akhozadi kukupulumutsani.