Chichewa Christian Hymns
Hymn 347 YESU, ndipemphera
YESU, ndipemphera
Mndithangate
Kukonda Inutu,
E, kwambiri.
Koposa zonsezo
Za pansi panopo,
Ndikondane
Ndinu Mbuye.
Kale ndinafuna
Za pansipa,
Tsopano ndilira
Inu nokha.
Ndifuna kukonda
Inu kopambana
Zinthu zonse
Za pansipa.
Inu ndidzatama
Nthaŵi zonse,
Imfa ikafika
Ndidzanena:
“Ndifuna kukonda
Inu, Mbuye wanga,
Kopambana
Zonse zanga.”