Chichewa Christian Hymns
Hymn 37 YESU analikhanda
YESU analikhanda
M’Betlehemumo;
M’ngelo anasimba za
Kubadwa kwake.
Kubadwa kwa Yesu
M’Betlehemumo;
Khandalo linagona
M’khola la ng’ombe.
Mngelo anatumidwa
Kuŵasimbira
Abusa a nkhosa za
Kubadwa kwake.
Anapita nasiya
Nkhosa zawozo;
Anapita kumudzi
Kukamlambira.
“Tadodoma, abusa,
Kwachitikanji?
Mwazisiyira yani
Nkhosa zanuzo?”
“Posunga nkhosa ife
Kubusa kwathu
Mngelo anasimba za
Kubadwa kwake.”