Chichewa Christian Hymns
Hymn 94 KHAMULO liliko
KHAMULO liliko
Kumwambako mbuu!
Pakukhala ndi Yesu
Aimbirako:
Kwa Iye atikonda
Natsuka ’fe mbuu!
E! kukhale ulemu
Kwa Mbuyathuyu.
Onsewa ’nachimwa
Nadetsedwa bii,
Nthaŵi yino ayera
Naimbiradi:
Akhala mafumu
Kwa Mbuyathuyo,
Anawombola onse
Ndi mwaziwo pyu!
Akadakhalabe
Osaukako
Ngati Yesu sakana
Wombolatuwo.
Ndi nyimbo yabwino
Tidzamtamako,
Kuti ena pakumva
Amuyimbirenso: