Chichewa Christian Hymns
Hymn 82 YANG’ANANI, anthu onse,
YANG’ANANI, anthu onse,
Yesu Mbuye wathuyo:
Alinkudza ndi ulemu,
Kuoneka m’Mwambamo.
Anthu onse am’lambire
Yesu Mwana wa Mulungu
Alinkudza ndi ulemu
Wopambana, indetu.
Adzatenga anthu ake
Akumvera pansipo
Iwo adzakhala naye
M’dziko la Kumwambako.
Koma anthu onse omwe
Anamnyoza pansipo,
Nthaŵi Yesu alinkudza
Adzaopa m’mtimamo.
Ife tonse tikumbuke
Mawu ake onsewo;
Timuyang’anire Iye,
Yesu Mbuye wathuyo.