Chichewa Christian Hymns
Hymn 79 PAKWITANA Mbuye wanga
PAKWITANA Mbuye wanga
Potsiriza dzikoli,
Pakufika tsiku la kuŵalalo,
Posonkhana akumvera,
Pakuona Yesuyo,
Ndidzakondwerera naye komweko.
Pakuyiitana Mbuye wanga,
Pakuyiitana Mbuye wanga,
Pakuyiitana Mbuye wanga,
Ndidzakondwerera naye komweko.
Potuluka m’manda mwawo
Anthu ake onsewo,
Tidzasanganatu nawo nthaŵiyo.
Pakuluka osankhidwa,
Kunka naye Yesuyo,
Ndidzakondwerera naye komweko.
Tisaleke kugwirabe
Ntchito ya Mulunguyo,
Tibukitse mbiri yake m’dzikoli,
Ndi podzatha moyo wathu
Ndi zintchito zathuzo,
Tidzakondwerera naye komweko.