Chichewa Christian Hymns
Hymn 76 E, MOYO wanga’we
E, MOYO wanga’we
Utsitsimuketu;
Ambuye Yesuyo
Akhala m’Mwambamo.
Pampandopo
Akhalabe, natchula dzina langali.
Kwa Mlungu m’Mwambamo
Amapempherako;
Chikondi chakenso
Chikhala chosatha;
Ndi mwaziwo
Akhalatu Wansembe wanga Yesuyo.
Mabala ajawo
A m’thupi mwakemo
Amukumbutsanso
Za ine pansipa;
Zoipazo
Achotsadi kotero sindingafe’yi
Mulungu ali wokhulula mtimatu,
Ndilibe mantha’yi,
Andisungiradi;
Ndibwera kwa
Atatewo, titayanjana leroli.