Chichewa Christian Hymns
Hymn 453 A! MULUNGU
A! MULUNGU
A! Mulungu
Anatuma mwana wake
Uja, ndiye Yesu
Anabadwa,
Anabadwa
Ndi Maria Mbeta ija
M’Betlehem muja.
Ndi angelo,
Ndi angelo
Anaimba: “Ndiye Yesu
Mpulumutsi wanu.”
Alanditsa,
Alanditsa
Ife anthu muzoipa
Zonse tazichita.
Yesu Mfumu
Yesu Mfumu,
Timagonja, mutisunge
Moyo wathu wonse.
Mutisuke,
Mutisuke
M’mwazi wanu, tikakhale
Ana anu tonse.