Chichewa Christian Hymns
Hymn 40 KAMWANA Yesu ’nabadwa,
KAMWANA Yesu ’nabadwa,
Ndi Iye Mlungu Wamphamvu;
Angelo anapembedza
Mwana wakhanda Iyeyu.
Kamwana kaja ’nayamba
Kuonetsera Atate,
Lero anena Kumwamba:
“Tiana tidze kwa Ine.”
Tibwera ndi tianato
Kukabatiza ’menewa;
Muŵachitire chifundo.
M’ŵapatse Mzimu Woyera.
Angelo anu asunga
Tiana tathu tofoka;
Pa njira yanu tiyenda,
Mulembe m’Mwamba maina.
Mukonda nyimbo za ana,
Kokoma amaimbatu;
Ndi ana athu atama
Atate, Mwana ndi Mzimu.