Chichewa Christian Hymns
Hymn 39 MUNASIYATU dziko lanulo,
MUNASIYATU dziko lanulo,
E, chifukwa cha íne;
Ndi ku Betlehemuko,
Pakubadwa Inu,
M’nyumba zawo nakukanani.
Mbuye Yesu, lowani ‘mtima,
Nyumba yanu ndi mtima’nga;
Mbuye Yesu, lowani ‘mtima,
Nyumba yanu ndi mtima’nga.
Akumwambako nayimbitsatu,
Kukulemekezaní;
Koma monga mwana,
M’dziko munabadwa,
Munadzíchepetsadi.
Nyama za mthengo ndi mbalamezo,
Zili namo mogonamo;
Koma Mwana Mlungu,
Analibe nyumba,
M’mapululu nagonatu.
Munadzera ndi mawu amoyo,
Akupulumutsa anthu;
Anakaníza,
Anasautsa,
Anapachika Inu.
Mmene mubwera kutiŵeruza,
Ndi angelo oyimbira;
Mundiitane,
Muti, “Idza ‘we,
Khala nane Kumwamba.”
Mtima wanga udzakondwera,
Mmene mundilandiranso;
Mtima wanga udzakondwera,
Mmene mundilandiranso.