Chichewa Christian Hymns
Hymn 386 MONGATU mawu anuwo,
MONGATU mawu anuwo,
Ndi Mtima chete phee,
Mbuyanga kufa kwanuko
Ndikumbukire ’ne.
Chakudya chakumwambachi
Ndi thupi lanudi;
Chikho cha chipanganochi
Ncha mwazi wanuwo.
Getsemane ndionako
Ndi nkhope yanu dwii,
Thukuta la pamphumilo
La myazi yanuyi.
Ndi mtanda uli m’maso mbuu,
Ndiona m’menemo,
A Yesu kufa kwanuko,
Kuthetsa imfazo.
Pamene padzakhalapo
Milomo yanga phee,
Mukadza ndi Ufumunso,
Mukumbukire ’ne.