Chichewa Christian Hymns
Hymn 36 AMBUYE tsopano lino, monga mwa mawu anu aja,
AMBUYE tsopano lino, monga mwa mawu anu aja,
Lolani kapolo wanu ndikachokere mumtendere;
Chifukwa chipulumutso chanu mwandionetsa zedi,
Chimene munachikonza akachione anthu onse;
Ndi nyali yakuŵalitsa omwe sadziŵa mawu anu;
Ndiwo ulemererowa Israyeli mpingo wanu.