Chichewa Christian Hymns
Hymn 334 KULI dziko labwino M’mwamba,
KULI dziko labwino M’mwamba,
Lakuwala koposa dzuwa;
Yesu watikonzera malo,
Pokhalira ife komweko.
Bwinoli tipita,
Tikomana mwa dziko lija;
Bwinoli tipita,
Tikomana mwa dziko lija.
Tidzayimba komweko nyimbo,
Za abwino omvera Yesu;
Sitidzamva chisoni ife,
Tidzakondwa masiku onse.
Tidzatama Atate wathu,
Kuti Iye ‘napatsa Yesu;
Kuchotsera zochimwa zonse,
Ndikutidalitsatu ife.