Chichewa Christian Hymns
Hymn 311 VALANI zida tizinka kwathuko,
VALANI zida tizinka kwathuko,
Tikayimbire Mulungu wa moyo;
Matupi athu adzasandulika,
Popita kwathuko.
Kwathu Kumwamba uko,
Moyo uliko uko;
Zowawa zonse uko kulibe,
Tidzayimbira pamodzi ndi Angelo,
Popita kwathuko.
Wotsogolera ndi Mbuye Yesuyo,
Paulendotu wopita kwathuko;
Tidzanyamula mbendera
Ya M’mwamba,
Popita kwathuko.
Pamene tonse tifika kwathuko,
Adzatipatsa korona wa moyo;
Tikayimbira Mulungu wa M’mwamba,
Pofika kwathuko.