Chichewa Christian Hymns
Hymn 299 TIYENI, Akristu inu,
TIYENI, Akristu inu,
Mumenyane nkhondo iyi,
Mukafoka nonse, koma
Yesu akulimbitsani.
Muyendanso kunka komwe,
Mugonjetse mdani wanu;
Musafoke, musaleme,
Musagone konse inu.
Musagonje, anthu inu,
Mtamiretu Yekha Mbuye;
Ipambana mphamvu yake,
Ya Mtsogoli wanu yemwe.
Mtima wanu wonse ndithu
Udzakhala ndi chimwemwe.
Zida zanu mbvale bwino
Zakudzera m’Mwamba momwe.
Limbikani inu nonse,
Msangalalo ngwanu nokha;
Musaope kanthu kena
Mumtamire Mbuye Yekha.
Tiyeni ku nkhondo iyi,
Mugonjetse zonse konko;
Muingitse mdani uja,
Muyendetse m’njira momwemo.