Chichewa Christian Hymns
Hymn 298 IFE tazingidwa ndi zinthu zoopsa,
IFE tazingidwa ndi zinthu zoopsa,
Zachisautso chomwechili nkudza;
Cha nambala ya a sikisi atatu;
Kodi tidzapiliradi?
Kodi inu mayi mudzapiliradi
Kuyenda inu wausiwa.
Kodi inu bambo mudzapiliradi
Panthawi ya masautsowo?
Zizindikirozo zili kuwoneka,
Kutitu nkhondoyo yayandikadi;
Tisakhaletu odabwitsika konse,
Tilimbike kupemphera.
Tidzawona ena a ifetu zedi,
Tili kudindidwa pamphumi pathu;
Tidziwetu kuti sitinalembedwe,
Mayina m’buku mulibe.