Chichewa Christian Hymns
Hymn 291 ULENDO wachikhrisitu ngosawutsa ndithu,
ULENDO wachikhrisitu ngosawutsa ndithu,
Mavuto, mayesero adza kwa ine;
Komatu ndidziŵitsitsa kuti Mbuye wanga,
Asunga moyo wanga kosalekeza.
Ndine wanu Mbuye wanga,
Mavuto, mayesero adza kwa ine;
Komatu ndidziwitsitsa
Kuti Mbuye wanga,
Asunga moyo wanga kosalekeza.
Chifukwa cha dzina lake
Ndanyozedwa ‘ne,
Adani achuluka, ndachepa ine;
Ndiwakonda onse
Koma andisautsa ‘ne,
Pukutani m’maso mwanga misoziyi.
Tiyeni abale tonse
Tilimbe ndithu,
Pogwira ntchito zake
Za Mbuye wathu;
Iye analonjezatu
Tsiku lomaliza,
Tidzakhala muulemelero wake.