Chichewa Christian Hymns
Hymn 28 AMBUYE ngwodalitsika,
AMBUYE ngwodalitsika,
Mulungu wa Israyeli ndiye,
Poti anayang’ana naŵawombola anthu ake,
Napulumutsa tonse mwapfuko la Davide mwana wake;
Monga analankhula mwa aneneri ake,
Adzatipulumutsa kudzanja la onse akutida,
Ndipo adzachitira akulu chifundo ndi chisoni.
Ndiye akumbukira pangani loyera lake lija,
Ndi chilumbiro chake cha kwa atate Abrahamu,
Choti timtumikire osaŵaopa ’dani athu,
Ndi kuyeranso mtima mwa chilungamo nsiku zonse.
Mwana, adzakuyesa mneneritu wa Wamkulukulu,
Ndiwe udzakonzera njira ya Mbuye Wakumwamba.
Udzadziŵitsa anthu za Mpulumutsi wawo yemwe
Aŵakhululukira
Nafafaniza tchimo lawo,
Poti Mulungu wathu ali ndi mtima wachifundo.
Ndiye kumwamba komwe
Ationetsa mbanda kucha,
Poŵalitsira omwe ali mumdima ndi muimfa,
Ndi potilunjikitsa tonse munjira yamtendere.