Chichewa Christian Hymns
Hymn 276 MKRISTU, ulimbike
MKRISTU, ulimbike
M’ntchito yakeyo;
Yesu anafera
Anthu akewo.
Mphamvu zathu zonse
Tionetsenso,
Kuti kudziŵike
Tili akewo.
Mtima wakufatsa
Amakondako;
Ndipo anthu onse
Angatengero.
Mapemphero athu
Tikakwezebe,
Dzina lake lomwe
Tiyamike ’fe.
Limbikani nonse
Mpaka imfayo.
Ndipo Mfumu yathu
Idzakondwatu.