Chichewa Christian Hymns
Hymn 243 KONDWANI nonsenu,
KONDWANI nonsenu,
Mpulumutsi anadza;
Onani kukhola,
Kumtanda ndi manda
Mlemekeze, bukitsani,
Naferatu kale;
Kondwerani, mlemekeze
Akhaladi moyo.
Kondwani nonsenu,
Anakhetsatu mwazi,
Natiwombola nawo,
Tikhale ana ’ke.
Kondwani nonsenu,
Atikhululukira,
Wosachimwa nafera
Anthu ’fe oipa.
Kondwani nonsenu,
Mfumu yathu yakwera;
Kwa Atate Kumwamba
Atipempherera.
Kondwani nonsenu,
Adzabweranso Yesu,
Waulemu, wamphamvu,
Kuweruza dziko.