Chichewa Christian Hymns
Hymn 216 NDISAUKA, ndinachimwa,
NDISAUKA, ndinachimwa,
Koma Inu m’nandifera;
Ndimo ndamva mund’itana,
Mwana Mlungu ndingobwera.
Ndisauka, ndimasowa,
Mphamvu yakuyera m’mtima;
Mwazi wanu wanditsuka,
Mwana Mlungu ndingobwera.
Ndisauka, sindikhoza,
Kuiletsa nkhondo m’ mtima;
Ndi chisoni, mantha nkhawa,
Mwana Mlungu ndingobwera.
Ndisauka, sindiona,
Ndingodwala, ndilefuka;
Zonse ndizitaya kwa ‘Nu,
Mwana Mlungu ndingobwera.
Inde, Yesu, mulandira,
Muchiritsa, m’ pulumutsa;
Mawu anu ndivomera,
Mwana Mlungu ndingobwera.
Inde, Yesu, mundikonda,
Zonse zina ndazitaya;
Tsono kukhala wanu,
Mwana Mlungu ndingobwera.