Chichewa Christian Hymns
Hymn 215 TATE ndili mwana wanu,
TATE ndili mwana wanu,
Nkana ndinachimwa,
Ndingolirira kwa Inu;
Khululukireni.
Machimo anga ngambiri
Osaŵerengeka,
Ndingoyang’ana kwa Inu;
Khululukireni.
Ndinachimwa poganiza
Ndi polankhulanso,
M’ntchito zanga ndachimwanso;
Khululukireni.
Ndinachita mphulupulu,
Ndinakunyozani,
M’ntchito zanga ndalephera;
Khululukireni.
Zonse ndinakonda kale
Ndi zopanda pake,
Sindinakhuta nazotu;
Khululukireni.