Chichewa Christian Hymns
Hymn 2 YEHOVA Mthandizi,
YEHOVA Mthandizi,
Wamoyo wanga pamavuto;
Amene muchotsa mantha,
Panthawi ya masautso.
Mufungatira moyotu wanga,
Panthawi ya masautso;
Mugwiritsitsa mzimutu wanga,
Panthawi ya masautso.
Yehova Mthandizi,
Wamoyo wanga poyesedwa;
Amene muchotsa mantha,
Panthawi ya masautso.
Yehova Mthandizi,
Wamoyo wanga pomwalira;
Amene muchotsa mantha,
Polowa m’dzenje la imfa.