Chichewa Christian Hymns
Hymn 191 AMBIRI tikondwera mwa Yesu,
AMBIRI tikondwera mwa Yesu,
Nanga inu? Nanga inu?
Tapeza chipulumutso ndithu;
Nanga inu?
Masiku onse timakondwera
Pakumva Mawu ake a Yesu;
Wolalikira tidzamumvera;
Nanga inu?
Ife tiyembekezera YESU,
Nanga inu? Nanga inu?
Chimwemwecho chilimumtimamu;
Nanga inu?
Titasokera tinabwerera,
Nanga inu? Nanga inu?
Tidziŵa kuti ndiwo uchimo;
Nanga inu?
Tinachoka munjira ya imfa,
Nanga inu? Nanga inu?
Takopeka ndi Mawu a Yesu;
Nanga inu?