Chichewa Christian Hymns
Hymn 167 KODI mwalandira Yesu?
KODI mwalandira Yesu?
Iye anakuferani.
Afunitsa inu nonse;
Kodi mumufunanso?
Kodi mufunatu Yesu?
Bvomerani msangatu:
“Inde Yesu ndifunadi,
Ndinu Mbuye wangatu.”
Nthaŵi zonse mufunabe
Zinthuzo za pansi pano;
Koma munyozabe Yesu
Wopachikidwa kalelo.
Yesu akuitanani
Kwanja kwake kwakukulu;
‘Mvani mawu ake lero,
Musachite nthantha’yi
Imfa idzafika msanga;
Ndipo mdzaikidwa m’manda;
Nthaŵi yomwe simudzamva
Kutitana kwakeko.