Chichewa Christian Hymns
Hymn 141 TAONANI pamtandapo,
TAONANI pamtandapo,
Natifera Mbuyeyo;
Tiyeni timuyamike,
Kaamba ka chifundocho.
Bwera kumtandawo
Mbuyeyo ayitana;
Bwera, zonse zakonzeka
Kodi ukulindanji?
Ndiye Mbusa wabwinoyo,
Wakuweta nkhosazo;
Yotayika ayifune,
Idzetu kwa Iyeyo.
Kodi mbale walandira,
Mwana wa Mulunguyo;
Mwina sunamulandire,
Kodi ukulindanji?