Chichewa Christian Hymns
Hymn 14 MTIMA wanga uyamike,
MTIMA wanga uyamike,
Mfumu ya Kumwambako,
Anandiwombola ine;
Nanditsuka m’mtimamo.
Ife tonse, ife tonse,
Tiyamike Mlunguyo.
Tiyamike Mulungu wathu,
Kaamba ka chifundocho;
Nthaŵi zonse sasinthika,
Mlungu wathu yemweyo.
Nthaŵi zonse monga Tate,
Atisamaliratu;
Atisunga m’manja mwake,
Atipulumutsatu.
Anthu a mitundu yonse,
Ndiponso a Kumwamba;
Yamikani Mungu wathu,
Ndiye wakukomatu.
Anthu onse, anthu onse,
Yamikani Mlunguyo.