Chichewa Christian Hymns
Hymn 129 WODALA ndiye munthuyo,
WODALA ndiye munthuyo,
Wosayenda moyipa;
Wosayimilira m’njira,
Ya anthu ochimwawo,
Ya anthu ochimwawo.
M’chilamulo cha Yehova,
Amakondwereramo;
Ndipo amalingilira,
Usana ndi usiku,
Usana ndi usiku.
Akunga mtengo wooka,
Pamitsinje yamadzi;
Chipatso chake chopatsa,
Panyengo yake yonse,
Panyengo yake yonse.
Kapena sakhala pansi,
Pabwalo la onyoza;
Zonse azichita iye,
Amapindula nazo,
Amapindula nazo.
Oyipa akunga mungu,
Wouluka ndi mphepo;
Mumsonkhano olungama,
Sadzaimilirako,
Sadzaimilirako.
Mayendedwe olungama,
Yehova awadziwa;
Koma oyipa onsewo,
Adzataika ndithu,
Adzataika ndithu.