Chichewa Christian Hymns
Hymn 115 NTHAWI ija ya Sauli,
NTHAWI ija ya Sauli,
Kunalitu nkhondo yoopsa;
Pakati pa Israyeli,
Ndi Afilisti.
Analimbanalimbana,
Afilisti nagonja,
Aisrayeli onse aja,
Nathamanga.
Ndipo Davide nafunsa,
“Munthu uyu ndiyetu yani;
Akunyoza makamuwo,
A Israyeli!”
Ndipo Davide natenga,
Kamwalako m’manja mwakemo;
Namulasa Goliyati,
Nagwa pansi.
Lero lino Mbuye Yesu,
Afunitsa inu ndi ine;
Tigonje pa mapazi ‘ke,
Ndikum’tsata.